22 Choncho Hilikiya ndi anthu amene mfumu inawatuma anapita kukalankhula ndi Hulida mneneri wamkazi.+ Hulida anali mkazi wa Salumu yemwe ankayangʼanira mosungira zovala, mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi. Hulidayo ankakhala Kumbali Yatsopano ya mzinda wa Yerusalemu.+