-
Nehemiya 8:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ezara anawerenga mokweza bukulo+ mʼbwalo lalikulu limene linali kutsogolo kwa Geti la Kumadzi, kuyambira mʼmawa mpaka masana. Anawerenga bukuli pamaso pa amuna, akazi ndiponso aliyense amene akanatha kumvetsa zimene zikunenedwa. Ndipo anthu ankamvetsera mwatcheru+ zimene zinali mʼbuku la Chilamuloli.
-