16 Asanamalize kulankhula, munthu wina anabwera nʼkunena kuti: “Moto wa Mulungu unatsika kuchokera kumwamba, ndipo unayaka pakati pa nkhosa ndi atumiki anu moti nkhosa komanso atumiki anuwo apsa. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka, choncho ndabwera kudzakuuzani uthengawu.”