3 Anthu ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana adzabwera nʼkunena kuti:
“Bwerani. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova,
Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+
Iye akatiphunzitsa njira zake,
Ndipo ife tidzayenda mʼnjira zakezo.”+
Chifukwa chilamulo chidzaphunzitsidwa mu Ziyoni,
Ndipo mawu a Yehova adzaphunzitsidwa mu Yerusalemu.+