7 Ndidzasokoneza zolinga za Yuda ndi za Yerusalemu mʼmalo ano, ndipo ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga la adani awo komanso ndi anthu amene akufunafuna moyo wawo. Mitembo yawo ndidzaipereka kwa mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakutchire kuti ikhale chakudya chawo.+