9 Ndidzawachititsa kudya mnofu wa ana awo aamuna ndi ana awo aakazi. Aliyense adzadya mnzake chifukwa adani adzawazungulira komanso chifukwa chosowa mtengo wogwira. Izi zidzachitika pamene adani awo ndiponso anthu amene akufuna moyo wawo adzawapanikize.”’+