5 Udzafa mu mtendere.+ Anthu adzakuchitira mwambo wowotcha zinthu zonunkhira ngati mmene anachitira ndi makolo ako, mafumu amene analipo iwe usanabadwe. Polira maliro ako adzanena kuti, ‘Mayo ine mbuyanga!’ chifukwa ‘Ine ndalankhula mawu amenewa,’ akutero Yehova.”’”’”