9 Inetu ndikuutsa gulu lalikulu la mitundu yamphamvu
Ndi kulibweretsa kuchokera kudziko lakumpoto kuti lidzaukire Babulo.+
Mitunduyi idzabwera ili yokonzeka kumenya nkhondo
Ndipo Babulo adzagonjetsedwa.
Mauta awo ndi ofanana ndi mauta a msilikali
Amene akupha ana.+
Iwo sabwerera asanachitepo kanthu.