13 Sheba+ ndi Dedani,+ amalonda a ku Tarisi+ ndi asilikali ake onse adzakufunsa kuti: “Kodi walowa mʼdzikoli kuti ukalande zinthu zambiri? Kodi wasonkhanitsa asilikali ako kuti ukatenge siliva, golide, chuma ndi katundu? Kodi ukufuna ukalande zinthu zambiri zamʼdzikoli?”’