6 Zipinda zamʼmbalizo zinali zosanjikizana katatu ndipo nsanjika iliyonse inali ndi zipinda 30. Kuzungulira khoma la kachisiyo panali timakonde timene tinali ngati maziko a zipinda zamʼmbali moti khoma la zipindazo linaima bwinobwino popanda kubowola khoma la kachisi.+