7 Kodi simunayenera kumvera mawu amene Yehova ananena kudzera mwa aneneri akale,+ pamene ku Yerusalemu ndi mizinda yozungulira kunkakhala anthu komanso kunali mtendere? Kodi simunayenera kumvera Mulungu pamene ku Negebu ndi ku Sefela kunkakhala anthu?’”