7 Kodi simunayenera kumvera mawu+ amene Yehova ananena kudzera mwa aneneri akale,+ pamene mu Yerusalemu ndi mizinda yake yonse yozungulira munali kukhala anthu, komanso pamene munali bata? Kodi simunayenera kumvera Mulungu pamene ku Negebu+ ndi ku Sefela+ kunali kukhala anthu?’”