6 Ndidzachititsa nyumba ya Yuda kukhala yapamwamba,
Ndipo nyumba ya Yosefe ndidzaipulumutsa.+
Ndidzawabwezera pamalo awo amene ankakhala,
Chifukwa ndidzawachitira chifundo.+
Iwo adzakhala ngati sanakanidwepo chiyambire.+
Popeza ine ndine Yehova Mulungu wawo, ndidzawayankha.