10 Iye anati: “Inu mwapatsidwa mwayi woti mumvetse zinsinsi zopatulika za Ufumu wa Mulungu. Koma kwa enawo, zonse ndi mafanizo okhaokha.+ Izi zili choncho kuti kuyangʼana aziyangʼana ndithu, koma kukhale kopanda phindu, kumvanso azimva ndithu, koma asamamvetse zimene zikunenedwa.+