48 Ndiyeno anawauza kuti: “Aliyense amene walandira mwana wamngʼono ngati uyu mʼdzina langa walandiranso ine. Ndipo aliyense amene walandira ine walandiranso amene anandituma.+ Chifukwa aliyense amene amachita zinthu ngati mwana wamngʼono pakati panu ndi amene ali wamkulu.”+