27 Choncho, ananyamuka nʼkupita ndipo anakumana ndi nduna ya ku Itiyopiya. Munthuyu anali ndi udindo waukulu ndipo ankathandiza Kandake, mfumukazi ya Itiyopiya. Ankayangʼaniranso chuma chonse cha mfumukaziyo. Iye anapita ku Yerusalemu kukalambira Mulungu.+