21 Komatu iwo anamva mphekesera zakuti iwe wakhala ukuphunzitsa Ayuda onse amene ali pakati pa anthu a mitundu ina kuti asiye kutsatira Chilamulo cha Mose. Akuti ukuwauza kuti asamachitenso mdulidwe wa ana awo komanso asamatsatire miyambo imene takhala tikuitsatira kuyambira kalekale.+