24 Utenge anthu amenewa ndipo ukachite nawo mwambo wa kudziyeretsa. Uwalipirire zonse zofunika, kuti amete tsitsi lawo. Ukatero, aliyense adziwa kuti mphekesera zimene anamva za iwe ndi nkhambakamwa chabe. Adzaona kuti ukuchita zinthu motsatira dongosolo komanso kuti umasunga Chilamulo.+