7 Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi Chilamulo ndi uchimo? Ayi ndithu. Kunena zoona, sindikanadziwa uchimo zikanakhala kuti panalibe Chilamulo.+ Mwachitsanzo, sindikanadziwa kusirira kwa nsanje zikanakhala kuti Chilamulo sichinanene kuti: “Usasirire mwansanje.”+