13 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti chinthu chabwino chinachititsa kuti ndife? Ayi. Uchimo ndi umene unachititsa kuti ndife. Chilamulo nʼchabwino, kungoti chinachititsa kuti zidziwike bwino kuti uchimo ukuchititsa kuti ndife.+ Choncho malamulo anatithandiza kudziwa kuti uchimo ndi woipa kwambiri.+