Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 11/1 tsamba 4-7
  • Dziko Lopanda Uchimo—Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lopanda Uchimo—Motani?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Uchimo Nchiyani?
  • Magwero a Uchimo
  • Zoyesayesa za Anthu Kufafaniza Uchimo
  • Kumasulidwa ku Uchimo
  • Pamene Sikudzakhalanso Uchimo
    Nsanja ya Olonda—1997
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amafa?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kuwomboledwa ndi ‘Mwazi wa Mtengo Wapatali’
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Tchimo
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 11/1 tsamba 4-7

Dziko Lopanda Uchimo​—Motani?

MFUU zogonthetsa zopempha chithandizo zinadodometsa bata la maola ammamaŵa wa tsiku lina la nyengo yachisanu m’chigawo chamtendere cha Tokyo. Anthu khumi ndi aŵiri anamva mfuu zosonyeza kuthedwa nzeru za mkazi wopereka mitokoma ya nyuzipepala akumathamangitsidwa kwa mphindi zoyambira pa zisanu kufikira khumi pamene anali kubaidwa mobwerezabwereza. Palibe ndi munthu mmodzi amene anasamala mokwanira kuti awone zimene zinali kuchitika. Mkaziyo anafa chifukwa cha kutaikiridwa ndi mwazi wochulukitsitsa. “Ngati mmodzi wa anthu ameneŵa akanachitira lipoti chochitikacho ku polisi mwamsanga pamene anamva kufuula kwake,” anatero wofufuzayo, “moyo wake ukanapulumutsidwa.”

Ngakhale kuti awo amene anali atamva mkazi womafayo sanachite chinthu choipirapo kwambiri kuposa kungonyalanyaza, kodi iwo moyenerera akanena kuti analibe liwongo? “Chikumbumtima changa chinandizunza tsiku lonse pa Lachisanu nditamva za kuphedwako,” anatero mwamuna wina amene anamva mfuu za mkaziyo. Zimenezi zimatipangitsa kufunsa kuti, Kodi kwenikweni uchimo nchiyani?

Kodi Uchimo Nchiyani?

Ponena za kuzindikiridwa kwa uchimo, Hideo Odagiri, katswiri m’kulemba mabukhu amenenso ali profesa wosagwiranso ntchito pa Yunivesite ya Hosei m’Tokyo, Japan, anati, malinga ndi mawu ake ogwidwa ndi nyuzipepala ya Asahi Shimbun akuti: “Sindingathe kufafaniza zikumbukiro zotsimikizirika zimene ndiri nazo za kuzindikiridwa kwa machimo, monga ngati kudzitukumula kwachabechabe kumene kumapezeka mwa mwana, nsanje yochititsa manyazi, kupereka munthu mobisa. Kuzindikira kumeneko kunakhomerezeka pa maganizo anga pamene ndinali ku sukulu yapulaimale ndipo kukadandivutitsabe.” Kodi inu munayamba mwakhalapo ndi malingaliro otero? Kodi muli ndi liwu m’kati mwanu limene limakutsutsani ngati muchita kanthu kena kamene mudziŵa kuti nkolakwa? Mwinamwake palibe upandu umene wachitidwa, koma lingaliro lokuvutitsani limakhalapobe ndi kusautsa kwambiri maganizo anu. Chimenechi ndicho chikumbumtima chanu chimene chikugwira ntchito, ndipo Baibulo limachitchula m’mawu otsatirawa: “Pamene anthu amitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo awonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana.” (Aroma 2:14, 15) Inde, mwachibadwa anthu ochuluka amavutitsidwa maganizo ndi machitidwe onga chigololo, kuba, ndi kunama. Chikumbumtima chawo chikuchitira umboni uchimo.

Komabe, pamene liwu lachikumbumtima linyalanyazidwa mobwerezabwereza, icho sichimatumikiranso monga chitsogozo chotetezera. Chingathe kukhala chosalabadira ndi choipitsidwa. (Tito 1:15) Kuzindikiridwa kwa choipa kumataika. M’chenicheni, lerolino chikumbumtima cha anthu ochuluka nchakufa pankhani ya uchimo.

Kodi chikumbumtima ndicho njira yokha yopimira uchimo, kapena kodi pali kanthu kena kamene kangatumikire monga muyezo weniweni ponena za chimene chiri uchimo ndi chimene uwo suuli? Koposa zaka 3,000 zapitazo, Mulungu anapereka kwa anthu ake osankhidwa mpambo wa malamulo, ndipo kupyolera mwa Chilamulo chimenechi, uchimo unafikira pa “kuzindikiridwa monga uchimo.” (Aroma 7:13, New International Version) Ngakhale mkhalidwe umene poyamba unawonekera ngati ngwovomerezedwa tsopano unavumbulutsidwa kukhala chimene uwo unali​—uchimo. Anthu osankhidwa a Mulungu, Aisrayeli, anavumbulidwa monga ochimwa ndipo monga otero anali otsutsidwa.

Kodi machimo ameneŵa ndiwo chiyani amene chikumbumtima chathu chimatizindikiritsa ndi amene Chilamulo cha Mose chinatchula ndi kundandalika? Kugwiritsidwa ntchito kwa liwulo m’Baibulo, uchimo umatanthauza kuphonya chandamale cha Mlengi. Chirichonse chosagwirizana ndi umunthu wake, miyezo, njira, ndi chifuniro ndicho uchimo. Iye sangathe kulola cholengedwa chirichonse chimene chimapereŵera pachandamale chimene iye waika kupitirizabe kukhala ndi moyo. Chotero katswiri wina wa lamulo m’zaka za zana loyamba anachenjeza Akristu Achihebri kuti: “Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo.” (Ahebri 3:12) Inde, kusakhala ndi chikhulupiriro mwa Mlengi ndiko tchimo lalikulu. Chotero, mlingo wauchimo monga momwe wafotokozedwera m’Baibulo ngwotakata kwambiri koposa chimene kaŵirikaŵiri chimalingaliridwa kukhala uchimo. Baibulo limafikira ngakhale pakufotokoza kuti: “Onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.”​—Aroma 3:23.

Magwero a Uchimo

Kodi izi zitanthauza kuti munthu analengedwa ali wochimwa? Ayi, Yehova Mulungu, Magwero a moyo waumunthu, anapanga munthu woyamba ali cholengedwa changwiro. (Genesis 1:26, 27; Deuteronomo 32:4) Komabe, okwatirana aŵiri oyamba anaphonya chandamalecho pamene ananyozera chiletso chimodzi chokha chimene Mulungu anapereka, pamene iwo anadya “mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa” woletsedwawo. (Genesis 2:17) Ngakhale kuti iwo analengedwa angwiro, iwo tsopano anaphonya chandamale cha kumvera kotheratu kwa Atate wawo, nakhala ochimwa, ndipo molondola anaweruzidwa ku imfa.

Kodi mbiri yakalekale imeneyi ikugwirizana pati ndi uchimo lerolino? Baibulo limafotokoza kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Tonsefe mosapatulapo aliyense tiri ochimwa mwacholowa; chifukwa chake, tinaloŵa m’chiweruzo cha imfa.​—Mlaliki 7:20.

Zoyesayesa za Anthu Kufafaniza Uchimo

Adamu anapitirizira uchimo kwa mbadwa zake, koma iye anapitiriziranso mphamvu ya chikumbumtima yoperekedwa ndi Mulungu. Uchimo ungachititse lingaliro lakutekeseka. Monga momwe kwatchulidwira kale, anthu ayesayesa kupeka njira zosiyanasiyana zofeŵetsera malingaliro otero. Komabe, kodi njirazo zimathandiza?

Kummaŵa ndi Kumadzulo, anthu ayesayesa kulimbana ndi chiyambukiro cha uchimo mwakusintha miyezo yawo kapena mwakulandula kukhalapo kwenikweniko kwa uchimo. (1 Timoteo 4:1, 2) Mkhalidwe wauchimo wa anthu ungayerekezeredwe ndi munthu wodwala malungo. Uchimo ungayerekezeredwe ndi kachilombo kamene kamachititsa kudwalako, pamene chikumbumtima chovutitsidwacho chikuyerekezeredwa ndi malungo ovutitsawo. Kuswa makina opimira kutentha ndi kuzizira kwa thupi sikumasintha chenicheni chakuti wodwalayo akudwala malungo aakulu. Kutaya miyezo yamakhalidwe abwino, monga momwe ambiri m’Chikristu Chadziko achitira, ndi kunyalanyaza umboni wa chikumbumtima cha munthuwe sindiko chithandizo m’kufafaniza uchimo weniweniwo.

Munthu angagwiritsire ntchito phukusi la aisi kuziziritsira malungo akewo. Kutero kuli kofanana ndi kuyesa kupoletsa zoŵaŵa za chikumbumtima kupyolera mwa zochitika za dzoma loyeretsa za Ashinto. Phukusi la aisi lingaziziritse kwakanthaŵi thupi la wodwala malungoyo, koma silimachotsa magwero amalungo. Ansembe ndi aneneri m’tsiku la Yeremiya anayesa kuchiritsa kofananako kwa Aisrayeli anthaŵi imeneyo. Iwo anachiritsa “pang’ono” mabala auzimu ndi amakhalidwe abwino a anthuwo, akumati, “zonse ziri bwino, zonse ziri bwino.” (Yeremiya 6:14; 8:11, An American Translation) Kugwiritsira ntchito kokha machitachita achipembedzo ndi kunenerera mawu onga akuti “zonse ziri bwino” sikunachiritse kusweka kwa makhalidwe abwino a anthu a Mulungu, ndipo madzoma oyeretsa samasintha miyambo ya anthu lerolino.

Mwakumwa mibulu yoziziritsa thupi lotentha munthu wodwala malungoyo angachititse malungo ake kuzilala, koma kachiromboko kadakali m’thupi lake. Zofananazo nzowona ndi njira Yachikonfyushasi yothetsera choipa kupyolera mwa maphunziro. Kunja kwake angawonekere kukhala akuthandiza anthu kupatuka pachoipa, koma kugwiritsira ntchito li kumangotsendereza kokha khalidwe lauchimo ndipo sikumachotsera munthuyo chikhoterero chake chauchimo chobadwa nacho, magwero aakulu akhalidwe lauchimo.​—Genesis 8:21.

Bwanji za chiphunzitso Chachibuddha chakuloŵa mu Nirvana kuti munthu adzichotsere zikhoterero zauchimo? Mkhalidwe wa Nirvana wonenedwa kutanthauza “kuzimitsa,” uyenera kukhala wosakhoza kufotokozedwa, kuzimitsidwa kwa zilakolako zonse ndi zikhumbo. Ena amanena kuti ndiko kuthetsedwa kwa kukhalapo kwa munthuyo. Kodi zimenezo sizimamvekera kukhala ngati kuuza munthu wodwala malungo kuti afe kotero kuti apeze mpumulo? Ndiponso, kufikira mkhalidwe wa Nirvana kukulingaliridwa kukhala kovuta kwambiri, ngakhale kosatheka. Kodi chiphunzitso chimenechi chikumvekera kukhala chothandiza kwa munthu wachikumbumtima chovutitsidwa?

Kumasulidwa ku Uchimo

Kuli kwachiwonekere kuti nthanthi za anthu zokhudza moyo ndi zikhoterero zauchimo kwakukulukulu zingathe kokha kutonthoza chikumbumtima cha munthuyo. Izo sizimachotsa mkhalidwe wauchimo. (1 Timoteo 6:20) Kodi pali njira iriyonse yakuchotsera mkhalidwe wauchimo? M’Baibulo, bukhu lakalekale lolembedwera ku Near East, timapezamo mfungulo yomasula ku uchimo. “Ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala . . . Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko.” (Yesaya 1:18, 19) Panopa Yehova anali kulankhula kwa Aisrayeli, amene, ngakhale kuti anali anthu ake osankhidwa, anali ataphonya chandamale cha umphumphu kwa iye. Komabe, lamulo la makhalidwe abwino lofananalo, limagwira ntchito kwa mtundu wonse wa anthu. Kusonyeza kufunitsitsa kumvetsera mawu a Mlengi ndiko mfungulo yakuchititsira machimo amunthuwe kuyeretsedwa, kutsukidwa, kunena kwake titero.

Kodi Mawu a Mulungu amatiuzanji ponena za kutsukidwa machimo kwa anthu? Monga momwedi mwauchimo wa munthu mmodzi anthu onse anakhala ochimwa, kupyolera mwa kumvera Mulungu kwangwiro kwa munthu wina, anthu omvera adzamasulidwa ku mavuto awo, Baibulo limatero. (Aroma 5:18, 19) Motani? “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m’menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” (Aroma 5:8) Yesu Kristu, monga munthu wobadwa wangwiro ndi wopanda uchimo, wolingana ndendende ndi Adamu woyambirira asanachimwe, anali mumkhalidwe wabwino wakusenza machimo a anthu. (Yesaya 53:12; Yohane 1:14; 1 Petro 2:24) Mwakuphedwera pa mtengo wozunzirapo monga ngati kuti anali mpandu, Yesu anamasula anthu ku ukapolo wauchimo ndi imfa. “Pakuti pamene,” anafotokoza motero Paulo kwa Akristu m’Roma, “tinali chikhalire ofoka, pa nyengo yake Kristu anawafera osapembedza. . . . kuti, monga uchimo unachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.”​—Aroma 5:6, 21.

Kufera anthu onse kochititdwa ndi Kristu ndi kubwezeretsa chimene Adamu anataya kumatchedwa kakonzedwe ka “dipo.” (Mateyu 20:28) Kungayerekezeredwe ndi mankhwala amene amapha kachirombo kochititsa malungo. Mwakugwiritsira ntchito mtengo wa dipo la Yesu kwa anthu, mkhalidwe wonga wakudwala wa anthuwo wochititsidwa ndi uchimo​—kuphatikizapo imfa yeniyeniyo​—ungachiritsidwe. Kachitidwe kakuchiritsa kameneka kafotokozedwa mophiphiritsira m’bukhu lomalizira la Baibulo kuti: “Tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziŵiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nawo amitundu.” (Chivumbulutso 22:2) Tangoyerekezerani! Mtsinje wophiphiritsira wa madzi amoyo ukuyenda tawatawa pakati pa mitengo yamoyo yokhala ndi masamba ake, zonsezo zochiritsira anthu. Zophiphiritsira zouziridwa ndi Mulungu zimenezi zimaimira kakonzedwe ka Mulungu kakubwezeretsera anthu kuungwiro pamaziko a nsembe ya dipo la Yesu.

Masomphenya aulosi a bukhu la Chivumbulutso adzakwaniritsidwa posachedwapa. (Chivumbulutso 22:6, 7) Pamenepo, mogwiritsira ntchito kotheratu mtengo wa nsembe ya dipo la Yesu kwa anthu, owongoka mtima onse adzafikira kukhala angwiro ndipo ‘adzamasulidwa ku ukapolo wachivundi ndi kulowa ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.’ (Aroma 8:21) Kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo kumasonyeza kuti chimasuko chaulemerero chimenechi chayandikira. (Chivumbulutso 6:1-8) Posachedwapa Mulungu adzachotsa kuipa pa dziko lapansi, ndipo anthu adzasangalala ndi moyo wamuyaya padziko lapansi la paradaiso. (Yohane 3:16) Limenelo lidzakhaladi dziko lopanda uchimo!

[Chithunzi patsamba 7]

Nsembe ya dipo la Yesu idzachititsa mabanja onga ili kusangalala ndi chimwemwe chosatha

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena