4 Koma nkhani imeneyi inayambika chifukwa cha abale achinyengo amene analowa pakati pathu mwakachetechete+ ndiponso mozemba ngati akazitape, nʼcholinga choti asokoneze ufulu+ umene tikusangalala nawo mogwirizana ndi Khristu Yesu, nʼkutisandutsa akapolo.+