13 ‘Ndikudziwa kumene ukukhala. Ukukhala kumene kuli mpando wachifumu wa Satana. Koma ukugwirabe mwamphamvu dzina langa+ ndipo sunakane kuti umandikhulupirira.+ Sunakane ngakhale mʼmasiku a Antipa, mboni yanga yokhulupirika,+ amene anaphedwa+ mumzinda wanu, kumene Satana akukhala.