12 “Kenako iye azitenga chofukizira+ chodzaza ndi makala amoto ochokera paguwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova. Azitenganso zofukiza zonunkhira zabwino kwambiri+ zokwana manja awiri+ odzaza, ndi kulowa nazo kuchipinda, kuseri kwa nsalu yotchinga.+