27 Koma nyama yodetsedwa+ yoyamba kubadwa angaiwombole. Ngati munthu akufuna kuiwombola azipereka mtengo wa nyamayo n’kuwonjezerapo limodzi mwa magawo asanu a mtengowo.+ Koma ngati mwiniwake wa nyamayo saiwombola wansembe aziigulitsa pa mtengo woikidwiratu.