17 Am’perekerenso nkhosa yamphongo monga nsembe yachiyanjano+ kwa Yehova, limodzi ndi dengu la mikate yopanda chofufumitsa ija. Kenako, wansembeyo apereke nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa, zimene zimayendera limodzi ndi nsembe yachiyanjanoyo.