12 “Ukamaliza kusonkhanitsa chakhumi chonse+ cha zokolola zako m’chaka chachitatu,+ chaka chopereka chakhumi, uzikapereka chakhumicho kwa Mlevi, mlendo wokhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye. Amenewa azidzadya ndi kukhuta chakhumicho m’mizinda yanu.+