12 Mukamaliza kusonkhanitsa chakhumi+ chonse cha zokolola zanu mʼchaka chachitatu, chaka chopereka chakhumi, muzikapereka chakhumicho kwa Mlevi, mlendo amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye ndipo azidzadya nʼkukhuta mʼmizinda yanu.+