8 Pamene anali pafupi ndi mwala waukulu umene uli ku Gibeoni,+ Amasa+ anabwera kudzakumana nawo. Tsopano Yowabu anali atavala malaya ankhondo ndi lamba. Iye anali ataika lupanga m’chimake ndi kulipachika m’chiuno mwake. Atayandikira Amasa, lupangalo linagwa pansi.