12 Ankachita izi Amasa ali chigonere pamagazi ake,+ pakati pa msewu waukulu. Mwamuna uja ataona kuti anthu onse akuima chilili, anakoka Amasa kumuchotsa pamsewu ndi kumuika patchire. Kenako anamuphimba ndi chovala pakuti anaona kuti aliyense amene anali kufika pamenepo anali kuima chilili.+