66 Pa tsiku la 8 Solomo anauza anthuwo kuti azipita,+ ndipo anthuwo anadalitsa mfumuyo n’kuyamba kupita kwawo. Anapita akusangalala,+ chimwemwe chitadzaza mumtima,+ chifukwa cha zabwino zonse+ zimene Yehova anachitira Davide mtumiki wake ndi anthu ake Aisiraeli.