10 Pakuti monga momwe mvula ndi chipale chofewa zimagwera kuchokera kumwamba, osabwereranso kumeneko mpaka zitanyowetsa kwambiri nthaka n’kumeretsa zomera ndi kuzibereketsa,+ wobzala mbewu n’kupatsidwa zokolola komanso wakudya n’kupatsidwa chakudya,+