26 “Tsopano imvani mawu a Yehova, inu nonse a ku Yuda amene mukukhala mu Iguputo muno.+ Yehova wanena kuti: “Ine ndalumbira m’dzina langa+ kuti m’dziko lonse la Iguputo simudzapezeka munthu aliyense wa ku Yuda woitanira pa dzina langa+ kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo, Ambuye Wamkulu Koposa!’+