7 Chotero ine ndinachita zonse monga mmene anandilamulira.+ Ndinatulutsa katundu wanga masana ngati mmene amachitira anthu opita ku ukapolo. Madzulo ndinaboola khoma ndi manja. Kutagwa mdima, ndinatulutsa katundu wanga, ndipo ndinanyamula katunduyo paphewa iwo akuona.