23 ‘Ndidzayeretsa dzina langa lalikulu+ limene linali kudetsedwa pakati pa mitundu ina ya anthu. Inu munadetsa dzina langalo pakati pa anthu a mitundu ina. Ndikadzayeretsedwa pakati panu, pamaso pa anthu a mitundu inawo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+