44 Kunja kwa kanyumba ka pachipata chamkati kunali zipinda zodyeramo oimba.+ Zipinda zimenezi zinali m’bwalo lamkati kumbali ya chipata cha kumpoto. Zipindazo zinayang’ana kum’mwera. Chipinda chimodzi chinali mbali ya kuchipata cha kum’mawa, ndipo chinayang’ana kumpoto.