9 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Limbani mtima anthu inu ndipo mukonzeke kugwira ntchito,+ inu amene mukumva mawu a aneneri masiku ano.+ Awa ndi mawu amene aneneriwo ananena pa tsiku limene maziko a nyumba ya Yehova wa makamu anayalidwa kuti kachisi amangidwe.+