37 “Yerusalemu, Yerusalemu, wakupha aneneri iwe+ ndi woponya miyala+ anthu otumizidwa kwa iwe.+ Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, muja nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko.+ Koma anthu inu simunafune zimenezo.+