11 Amunawo anawafunsa kuti: “Amuna inu a ku Galileya, n’chifukwa chiyani muli chilili choncho kuyang’ana kuthambo? Yesu ameneyu, amene watengedwa kupita kumwamba kuchoka pakati panu, adzabwera m’njira yofanana+ ndi mmene mwamuonera akukwera kuthambo.”