5 Koma Ayuda anachita nsanje,+ ndipo anatengana ndi anthu ena oipa, anthu osowa chochita amene anali kungokhala pamsika. Iwowa anapanga gulu lachiwawa ndi kuyambitsa chipolowe mumzindamo.+ Kenako anakhamukira kunyumba ya Yasoni,+ kukafuna atumwiwo kuti awatulutsire ku gulu lachipolowelo.