14 Komatu ndikuvomereza izi kwa inu: Njira yolambirira imene iwo akuitcha ‘gulu lampatuko,’ ndi njira imene ine ndikuchitira utumiki wopatulika kwa Mulungu wa makolo anga.+ Pakuti ndimakhulupirira zonse zimene zili m’Chilamulo+ ndi Zolemba za aneneri.