5 Zoonadi, amuna ochokera mwa ana aamuna a Levi,+ amene amalandira udindo wa unsembe, amalamulidwa kulandira zakhumi+ kuchokera kwa anthu+ malinga ndi Chilamulo. Izi zikutanthauza kuti, amalandira zakhumizo kuchokera kwa abale awo, ngakhale kuti abale awowo anachokera m’chiuno mwa Abulahamu.+