19 Pakuti pamene Mose anatchulira anthu onsewo lamulo lililonse malinga ndi Chilamulo,+ anatenga magazi a ng’ombe zazing’ono zamphongo ndi magazi a mbuzi, pamodzi ndi madzi, ubweya wa nkhosa wofiira kwambiri, ndi timitengo ta hisope,+ n’kuwaza bukulo ndi anthu onse.