Lachiwiri, October 21
Amene adzapirire mpaka pamapeto ndi amene adzapulumuke.—Mat. 24:13.
Muziganizira ubwino wokhala woleza mtima. Tikakhala oleza mtima timakhala osangalala komanso odekha. Ndipotu kukhala ndi khalidweli kungatithandize kuti tiziganiza bwino komanso tikhale ndi thanzi labwino. Tikamachita zinthu moleza mtima ndi ena, timakhala nawo pa ubwenzi wabwino. Timakhalanso ogwirizana kwambiri mumpingo. Ngati wina watikhumudwitsa sitimakwiya msanga, zomwe zimachititsa kuti zinthu zisaipe kwambiri. (Sal. 37:8; Miy. 14:29) Koposa zonse, timakhala tikutsanzira Atate wathu wakumwamba ndipo timakhala naye pa ubwenzi wabwino kwambiri. Kunena zoona, kuleza mtima ndi khalidwe losangalatsa komanso lothandiza kwambiri. N’zoona kuti si nthawi zonse pamene kuleza mtima kungakhale kophweka. Koma mothandizidwa ndi Yehova, tikhoza kupitiriza kukhala ndi khalidweli. Pamene tikuyembekezera moleza mtima dziko latsopano, tisamakayikire kuti “Diso la Yehova limayang’ana anthu amene amamuopa, amene amayembekezera chikondi chake chokhulupirika.” (Sal. 33:18) Tiyeni tonse tikhale otsimikiza mtima kuti tipitirizabe kukhala oleza mtima. w23.08 22 ¶7; 25 ¶16-17
Lachitatu, October 22
Chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa.—Yak. 2:17.
Yakobo ananena kuti munthu angamanene kuti ali ndi chikhulupiriro, koma zochita zake sizikusonyeza zimenezo. (Yak. 2:1-5, 9) Yakobo anafotokozanso za munthu yemwe anaona “m’bale kapena mlongo alibe zovala” koma sanamuthandize. Ngakhale munthu ameneyu atamanena kuti ali ndi chikhulupiriro, zingakhale zosamveka. (Yak. 2:14-16) Yakobo anatchula Rahabi monga chitsanzo cha munthu yemwe anasonyeza chikhulupiriro mwa zochita zake. (Yak. 2:25, 26) Iye anali atamva zokhudza Yehova ndiponso kuti ndi yemwe ankathandiza Aisiraeli. (Yos. 2:9-11) Rahabi anasonyeza chikhulupiriro mwa zochita zake poteteza Aisiraeli awiri omwe anabwera kudzafufuza dziko lawo ndipo moyo wawo unali pangozi. Izi zinachititsa kuti mayi wochimwayu, yemwenso sanali Mwisiraeli, aonedwe kuti ndi wolungama ngati mmene Abulahamu analili. Chitsanzo chake chimasonyeza kufunika kokhala ndi chikhulupiriro komanso ntchito zake. w23.12 5-6 ¶12-13
Lachinayi, October 23
Muzike mizu ndiponso mukhale okhazikika pamaziko.—Aef. 3:17.
Monga Akhristu, sitimangokhutira ndi kumvetsa mfundo zoyambirira za m’Baibulo. Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, timafunitsitsanso kudziwa “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:9, 10) Bwanji osakonza zoti mufufuze mozama zinthu zomwe zingakuthandizeni kuti mukhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Mwachitsanzo, mungafufuze mmene anasonyezera kuti ankakonda atumiki ake akale komanso mmene zimenezo zimasonyezera kuti inunso amakukondani. Mungaphunzirenso zimene Yehova ankafuna kuti Aisiraeli azichita pomulambira n’kuziyerekezera ndi zimene amafuna kuti ifenso tizichita pomulambira masiku ano. Kapenanso mungaphunzire mozama zokhudza maulosi amene Yesu anakwaniritsa pa utumiki wake padziko lapansi. Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani lingakuthandizeni kuti muzisangalala pophunzira. Kuphunzira Baibulo mozama kungalimbitse chikhulupiriro chanu komanso kungakuthandizeni kuti ‘mumudziwedi Mulungu.’—Miy. 2:4, 5 w23.10 18-19 ¶3-5