Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Lolemba, October 20

Ngati simundiuza zimene ndalota n’kundimasulira, ndikudulani nthulinthuli.​—Dan. 2:5.

Patatha zaka pafupifupi ziwiri kuchokera pamene Ababulo anawononga mzinda wa Yerusalemu, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inasokonezeka maganizo ndi zimene inalota zokhudza chifaniziro chachikulu kwambiri. Mfumuyi inaopseza kuti ipha amuna onse anzeru kuphatikizapo Danieli ngati sakanaiuza zomwe inalota komanso kumasulira kwake. (Dan. 2:3-5) Danieli ankafunika kuchitapo kanthu mwamsanga chifukwa ngati sakanatero anthu ambiri akanaphedwa. Iye “anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulire maloto ake.” (Dan. 2:16) Apatu anasonyeza kulimba mtima komanso chikhulupiriro. Palibe paliponse pamene pamasonyeza kuti Danieli anali atamasulirapo maloto. Iye anapempha anzake kuti “apemphere kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo n‘kuwaululira chinsinsi chimenechi.” (Dan. 2:18) Yehova anayankha mapemphero amenewo. Mothandizidwa ndi Mulungu, Danieli anamasulira maloto a Nebukadinezara ndipo iye ndi anzake sanaphedwe. w23.08 3 ¶4

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachiwiri, October 21

Amene adzapirire mpaka pamapeto ndi amene adzapulumuke.​—Mat. 24:13.

Muziganizira ubwino wokhala woleza mtima. Tikakhala oleza mtima timakhala osangalala komanso odekha. Ndipotu kukhala ndi khalidweli kungatithandize kuti tiziganiza bwino komanso tikhale ndi thanzi labwino. Tikamachita zinthu moleza mtima ndi ena, timakhala nawo pa ubwenzi wabwino. Timakhalanso ogwirizana kwambiri mumpingo. Ngati wina watikhumudwitsa sitimakwiya msanga, zomwe zimachititsa kuti zinthu zisaipe kwambiri. (Sal. 37:8; Miy. 14:29) Koposa zonse, timakhala tikutsanzira Atate wathu wakumwamba ndipo timakhala naye pa ubwenzi wabwino kwambiri. Kunena zoona, kuleza mtima ndi khalidwe losangalatsa komanso lothandiza kwambiri. N’zoona kuti si nthawi zonse pamene kuleza mtima kungakhale kophweka. Koma mothandizidwa ndi Yehova, tikhoza kupitiriza kukhala ndi khalidweli. Pamene tikuyembekezera moleza mtima dziko latsopano, tisamakayikire kuti “Diso la Yehova limayang’ana anthu amene amamuopa, amene amayembekezera chikondi chake chokhulupirika.” (Sal. 33:18) Tiyeni tonse tikhale otsimikiza mtima kuti tipitirizabe kukhala oleza mtima. w23.08 22 ¶7; 25 ¶16-17

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachitatu, October 22

Chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa.​—Yak. 2:17.

Yakobo ananena kuti munthu angamanene kuti ali ndi chikhulupiriro, koma zochita zake sizikusonyeza zimenezo. (Yak. 2:1-5, 9) Yakobo anafotokozanso za munthu yemwe anaona “m’bale kapena mlongo alibe zovala” koma sanamuthandize. Ngakhale munthu ameneyu atamanena kuti ali ndi chikhulupiriro, zingakhale zosamveka. (Yak. 2:14-16) Yakobo anatchula Rahabi monga chitsanzo cha munthu yemwe anasonyeza chikhulupiriro mwa zochita zake. (Yak. 2:25, 26) Iye anali atamva zokhudza Yehova ndiponso kuti ndi yemwe ankathandiza Aisiraeli. (Yos. 2:9-11) Rahabi anasonyeza chikhulupiriro mwa zochita zake poteteza Aisiraeli awiri omwe anabwera kudzafufuza dziko lawo ndipo moyo wawo unali pangozi. Izi zinachititsa kuti mayi wochimwayu, yemwenso sanali Mwisiraeli, aonedwe kuti ndi wolungama ngati mmene Abulahamu analili. Chitsanzo chake chimasonyeza kufunika kokhala ndi chikhulupiriro komanso ntchito zake. w23.12 5-6 ¶12-13

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena