Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Lamlungu, October 19

Muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.​—Luka 5:4.

Yesu anatsimikizira mtumwi Petulo kuti Yehova adzamuthandiza. Iye ataukitsidwa anathandiza Petulo ndi atumwi anzake kuphanso nsomba m’njira yodabwitsa. (Yoh. 21:4-6) Mosakayikira zimenezi zinatsimikizira Petulo kuti Yehova angamuthandize kupeza zofunika pa moyo. N’kutheka kuti mtumwiyu anakumbukira zimene Yesu ananena kuti Yehova adzathandiza aliyense amene amapitiriza ‘kuika Ufumu pamalo oyamba’. (Mat. 6:33) Zonsezi zinathandiza Petulo kuti aziona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri kuposa usodzi. Pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E., iye analalikira molimba mtima ndipo anathandiza anthu ambiri kuti amve uthenga wabwino. (Mac. 2:14, 37-41) Pambuyo pake anathandiza Asamariya komanso anthu amitundu ina kuti ayambe kukhulupirira Khristu. (Mac. 8:14-17; 10:44-48) Apatu Yehova anagwiritsa ntchito kwambiri Petulo kuti athandize anthu a mitundu yonse kuti abwere mumpingo wa Chikhristu. w23.09 20 ¶1; 23 ¶11

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lolemba, October 20

Ngati simundiuza zimene ndalota n’kundimasulira, ndikudulani nthulinthuli.​—Dan. 2:5.

Patatha zaka pafupifupi ziwiri kuchokera pamene Ababulo anawononga mzinda wa Yerusalemu, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inasokonezeka maganizo ndi zimene inalota zokhudza chifaniziro chachikulu kwambiri. Mfumuyi inaopseza kuti ipha amuna onse anzeru kuphatikizapo Danieli ngati sakanaiuza zomwe inalota komanso kumasulira kwake. (Dan. 2:3-5) Danieli ankafunika kuchitapo kanthu mwamsanga chifukwa ngati sakanatero anthu ambiri akanaphedwa. Iye “anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulire maloto ake.” (Dan. 2:16) Apatu anasonyeza kulimba mtima komanso chikhulupiriro. Palibe paliponse pamene pamasonyeza kuti Danieli anali atamasulirapo maloto. Iye anapempha anzake kuti “apemphere kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo n‘kuwaululira chinsinsi chimenechi.” (Dan. 2:18) Yehova anayankha mapemphero amenewo. Mothandizidwa ndi Mulungu, Danieli anamasulira maloto a Nebukadinezara ndipo iye ndi anzake sanaphedwe. w23.08 3 ¶4

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachiwiri, October 21

Amene adzapirire mpaka pamapeto ndi amene adzapulumuke.​—Mat. 24:13.

Muziganizira ubwino wokhala woleza mtima. Tikakhala oleza mtima timakhala osangalala komanso odekha. Ndipotu kukhala ndi khalidweli kungatithandize kuti tiziganiza bwino komanso tikhale ndi thanzi labwino. Tikamachita zinthu moleza mtima ndi ena, timakhala nawo pa ubwenzi wabwino. Timakhalanso ogwirizana kwambiri mumpingo. Ngati wina watikhumudwitsa sitimakwiya msanga, zomwe zimachititsa kuti zinthu zisaipe kwambiri. (Sal. 37:8; Miy. 14:29) Koposa zonse, timakhala tikutsanzira Atate wathu wakumwamba ndipo timakhala naye pa ubwenzi wabwino kwambiri. Kunena zoona, kuleza mtima ndi khalidwe losangalatsa komanso lothandiza kwambiri. N’zoona kuti si nthawi zonse pamene kuleza mtima kungakhale kophweka. Koma mothandizidwa ndi Yehova, tikhoza kupitiriza kukhala ndi khalidweli. Pamene tikuyembekezera moleza mtima dziko latsopano, tisamakayikire kuti “Diso la Yehova limayang’ana anthu amene amamuopa, amene amayembekezera chikondi chake chokhulupirika.” (Sal. 33:18) Tiyeni tonse tikhale otsimikiza mtima kuti tipitirizabe kukhala oleza mtima. w23.08 22 ¶7; 25 ¶16-17

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena