Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Loweruka, October 18

Pitirizani kupempha ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitirizani kugogoda ndipo adzakutsegulirani.​—Luka 11:9.

Kodi mukufuna muzisonyeza kuleza mtima kwambiri? Ngati ndi choncho, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Kuleza mtima ndi limodzi mwa makhalidwe omwe mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Choncho tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu wake kuti tikhale ndi makhalidwe omwe umatulutsa. Ngati tikuyesedwa pa nkhani yokhala oleza mtima, tiyenera ‘kupitiriza kupempha’ mzimu woyera kuti utithandize kukhala oleza mtima. (Luka 11:13) Tingapemphenso Yehova kuti atithandize kuti tiziona zinthu mmene iyeyo amazionera. Kenako pambuyo popemphera, tizichita zomwe tingathe kuti tizikhala oleza mtima tsiku lililonse. Tikamapemphera kwambiri kuti tikhale oleza mtima n’kumayesetsa kusonyeza khalidweli, m’pamenenso limakhazikika kwambiri mumtima ndipo limangokhala ngati mbali ya moyo wathu. Chinanso chomwe chingatithandize ndi kuganizira mozama za anthu otchulidwa m’Baibulo. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe anali oleza mtima. Tikhoza kuphunzira mmene tingasonyezere kuleza mtima tikamaganizira kwambiri zitsanzozi. w23.08 22 ¶10-11

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lamlungu, October 19

Muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.​—Luka 5:4.

Yesu anatsimikizira mtumwi Petulo kuti Yehova adzamuthandiza. Iye ataukitsidwa anathandiza Petulo ndi atumwi anzake kuphanso nsomba m’njira yodabwitsa. (Yoh. 21:4-6) Mosakayikira zimenezi zinatsimikizira Petulo kuti Yehova angamuthandize kupeza zofunika pa moyo. N’kutheka kuti mtumwiyu anakumbukira zimene Yesu ananena kuti Yehova adzathandiza aliyense amene amapitiriza ‘kuika Ufumu pamalo oyamba’. (Mat. 6:33) Zonsezi zinathandiza Petulo kuti aziona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri kuposa usodzi. Pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E., iye analalikira molimba mtima ndipo anathandiza anthu ambiri kuti amve uthenga wabwino. (Mac. 2:14, 37-41) Pambuyo pake anathandiza Asamariya komanso anthu amitundu ina kuti ayambe kukhulupirira Khristu. (Mac. 8:14-17; 10:44-48) Apatu Yehova anagwiritsa ntchito kwambiri Petulo kuti athandize anthu a mitundu yonse kuti abwere mumpingo wa Chikhristu. w23.09 20 ¶1; 23 ¶11

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lolemba, October 20

Ngati simundiuza zimene ndalota n’kundimasulira, ndikudulani nthulinthuli.​—Dan. 2:5.

Patatha zaka pafupifupi ziwiri kuchokera pamene Ababulo anawononga mzinda wa Yerusalemu, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inasokonezeka maganizo ndi zimene inalota zokhudza chifaniziro chachikulu kwambiri. Mfumuyi inaopseza kuti ipha amuna onse anzeru kuphatikizapo Danieli ngati sakanaiuza zomwe inalota komanso kumasulira kwake. (Dan. 2:3-5) Danieli ankafunika kuchitapo kanthu mwamsanga chifukwa ngati sakanatero anthu ambiri akanaphedwa. Iye “anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulire maloto ake.” (Dan. 2:16) Apatu anasonyeza kulimba mtima komanso chikhulupiriro. Palibe paliponse pamene pamasonyeza kuti Danieli anali atamasulirapo maloto. Iye anapempha anzake kuti “apemphere kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo n‘kuwaululira chinsinsi chimenechi.” (Dan. 2:18) Yehova anayankha mapemphero amenewo. Mothandizidwa ndi Mulungu, Danieli anamasulira maloto a Nebukadinezara ndipo iye ndi anzake sanaphedwe. w23.08 3 ¶4

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena