Lachisanu, October 17
Pitirizani kuyenda ngati ana a kuwala.—Aef. 5:8.
Timafunika mzimu woyera wa Mulungu kuti tipitirize kuchita zinthu ngati “ana a kuwala.” Chifukwa chiyani? Chifukwa si zophweka kupitiriza kukhala oyera m’dziko la makhalidwe oipali. (1 Ates. 4:3-5, 7, 8) Mzimu woyera ungatithandize kupewa maganizo a m’dzikoli kuphatikizapo nzeru za anthu komanso mfundo zimene zimasemphana ndi maganizo a Mulungu. Ungatithandizenso kuti tizichita ‘chilichonse chabwino ndi chilichonse cholungama.’ (Aef. 5:9) Njira imodzi imene tingalandirire mzimu woyera ndi kuupempha. Yesu ananena kuti Yehova “adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akumupempha.” (Luka 11:13) Komanso tikamatamanda Yehova pamisonkhano ndi Akhristu anzathu timalandira mzimu woyera. (Aef. 5:19, 20) Mzimu woyera umatithandiza kuti tizichita zinthu zimene zimasangalatsa Mulungu. w24.03 23-24 ¶13-15
Loweruka, October 18
Pitirizani kupempha ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitirizani kugogoda ndipo adzakutsegulirani.—Luka 11:9.
Kodi mukufuna muzisonyeza kuleza mtima kwambiri? Ngati ndi choncho, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Kuleza mtima ndi limodzi mwa makhalidwe omwe mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Choncho tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu wake kuti tikhale ndi makhalidwe omwe umatulutsa. Ngati tikuyesedwa pa nkhani yokhala oleza mtima, tiyenera ‘kupitiriza kupempha’ mzimu woyera kuti utithandize kukhala oleza mtima. (Luka 11:13) Tingapemphenso Yehova kuti atithandize kuti tiziona zinthu mmene iyeyo amazionera. Kenako pambuyo popemphera, tizichita zomwe tingathe kuti tizikhala oleza mtima tsiku lililonse. Tikamapemphera kwambiri kuti tikhale oleza mtima n’kumayesetsa kusonyeza khalidweli, m’pamenenso limakhazikika kwambiri mumtima ndipo limangokhala ngati mbali ya moyo wathu. Chinanso chomwe chingatithandize ndi kuganizira mozama za anthu otchulidwa m’Baibulo. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe anali oleza mtima. Tikhoza kuphunzira mmene tingasonyezere kuleza mtima tikamaganizira kwambiri zitsanzozi. w23.08 22 ¶10-11
Lamlungu, October 19
Muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.—Luka 5:4.
Yesu anatsimikizira mtumwi Petulo kuti Yehova adzamuthandiza. Iye ataukitsidwa anathandiza Petulo ndi atumwi anzake kuphanso nsomba m’njira yodabwitsa. (Yoh. 21:4-6) Mosakayikira zimenezi zinatsimikizira Petulo kuti Yehova angamuthandize kupeza zofunika pa moyo. N’kutheka kuti mtumwiyu anakumbukira zimene Yesu ananena kuti Yehova adzathandiza aliyense amene amapitiriza ‘kuika Ufumu pamalo oyamba’. (Mat. 6:33) Zonsezi zinathandiza Petulo kuti aziona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri kuposa usodzi. Pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E., iye analalikira molimba mtima ndipo anathandiza anthu ambiri kuti amve uthenga wabwino. (Mac. 2:14, 37-41) Pambuyo pake anathandiza Asamariya komanso anthu amitundu ina kuti ayambe kukhulupirira Khristu. (Mac. 8:14-17; 10:44-48) Apatu Yehova anagwiritsa ntchito kwambiri Petulo kuti athandize anthu a mitundu yonse kuti abwere mumpingo wa Chikhristu. w23.09 20 ¶1; 23 ¶11