Lachinayi, August 28
Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana, onse amene amamuitana mʼchoonadi.—Sal. 145:18.
Yehova “Mulungu amene ndi wachikondi,” ali nafe. (2 Akor. 13:11) Iye amakonda munthu aliyense payekha. Sitimakayikira kuti nthawi zonse amatisonyeza “chikondi chake chokhulupirika.” (Sal. 32:10) Tikamaganizira kwambiri mmene amasonyezera chikondi chake kwa ife, m’pamenenso timakhala naye pa ubwenzi wolimba kwambiri. Tingathe kupemphera kwa iye momasuka ndi kumufotokozera mmene timayamikirira chikondi chake. Tingamamufotokozerenso zonse zimene zikutidetsa nkhawa n’kumakhulupirira kuti amatimvetsa ndiponso ndi wofunitsitsa kutithandiza. (Sal. 145:19) Tonsefe timakopeka ndi chikondi cha Yehova ngati mmene timachitira ndi moto pa tsiku limene kukuzizira. Chikondi cha Yehova ndi champhamvu koma amachisonyezanso mokoma mtima. Choncho muzisangalala chifukwa Yehova amakukondani. Zimenezi zizitichititsa tonsefe kunena mosangalala kuti: “Ndimakonda Yehova.”—Sal. 116:1. w24.01 31 ¶19-20
Lachisanu, August 29
Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu.—Yoh. 17:26.
Yesu anachita zambiri kuposa kungodziwitsa anthu kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Ayuda omwe ankawaphunzitsa, ankadziwa kale dzina la Mulungu. Koma Yesu anapereka chitsanzo chabwino chifukwa “ndi amene anafotokoza za Mulungu.” (Yoh. 1:17, 18) Mwachitsanzo, Malemba a Chiheberi amasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima. (Eks. 34:5-7) Yesu anamveketsa bwino mfundo ya choonadi imeneyi pamene anafotokoza fanizo la mwana wolowerera ndi bambo ake. Tikamawerenga zimene bamboyu anachita ataona mwana wake wolapayo “ali chapatali ndithu,” n’kumuthamangira, kumukumbatira komanso kumukhululukira ndi mtima wonse, timamvetsa bwino chifundo komanso kukoma mtima kwa Yehova. (Luka 15:11-32) Apa Yesu anathandiza anthu kumvetsa zoona zenizeni zokhudza mmene Atate wake alili. w24.02 10 ¶8-9
Loweruka, August 30
Tizitonthoza [ena] . . . chifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.—2 Akor. 1:4.
Yehova amatsitsimula komanso kutonthoza anthu omwe akumana ndi mavuto. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova potonthoza ena komanso kusonyeza chifundo? Tingachite zimenezi poyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene angatithandize kuti titonthoze anthu ena. Kodi ena mwa makhalidwe amenewa ndi ati? Nanga n’chiyani chingatithandize kukhala ndi chikondi chimene chimafunika kuti tizitonthozana kapena kuti “kulimbikitsana” tsiku ndi tsiku? (1 Ates. 4:18) Tiyenera kukhala ndi makhalidwe monga kumvera ena chisoni, kukonda abale komanso kukoma mtima. (Akol. 3:12; 1 Pet. 3:8) Kodi makhalidwe amenewa angatithandize bwanji? Tikamakhala ndi chifundo komanso makhalidwe amene tatchulawa, sitingachitire mwina koma kutonthoza ena. Paja Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chabwino chamumtima mwake, koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’chuma choipa chamumtima mwake.” (Mat. 12:34, 35) Kutonthoza abale ndi alongo athu omwe akumana ndi mavuto ndi njira yofunika kwambiri yomwe tingasonyezere kuti timawakonda. w23.11 10 ¶10-11