Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Lachisanu, August 29

Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu.​—Yoh. 17:26.

Yesu anachita zambiri kuposa kungodziwitsa anthu kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Ayuda omwe ankawaphunzitsa, ankadziwa kale dzina la Mulungu. Koma Yesu anapereka chitsanzo chabwino chifukwa “ndi amene anafotokoza za Mulungu.” (Yoh. 1:17, 18) Mwachitsanzo, Malemba a Chiheberi amasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima. (Eks. 34:5-7) Yesu anamveketsa bwino mfundo ya choonadi imeneyi pamene anafotokoza fanizo la mwana wolowerera ndi bambo ake. Tikamawerenga zimene bamboyu anachita ataona mwana wake wolapayo “ali chapatali ndithu,” n’kumuthamangira, kumukumbatira komanso kumukhululukira ndi mtima wonse, timamvetsa bwino chifundo komanso kukoma mtima kwa Yehova. (Luka 15:11-32) Apa Yesu anathandiza anthu kumvetsa zoona zenizeni zokhudza mmene Atate wake alili. w24.02 10 ¶8-9

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Loweruka, August 30

Tizitonthoza [ena] . . . chifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.​—2 Akor. 1:4.

Yehova amatsitsimula komanso kutonthoza anthu omwe akumana ndi mavuto. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova potonthoza ena komanso kusonyeza chifundo? Tingachite zimenezi poyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene angatithandize kuti titonthoze anthu ena. Kodi ena mwa makhalidwe amenewa ndi ati? Nanga n’chiyani chingatithandize kukhala ndi chikondi chimene chimafunika kuti tizitonthozana kapena kuti “kulimbikitsana” tsiku ndi tsiku? (1 Ates. 4:18) Tiyenera kukhala ndi makhalidwe monga kumvera ena chisoni, kukonda abale komanso kukoma mtima. (Akol. 3:12; 1 Pet. 3:8) Kodi makhalidwe amenewa angatithandize bwanji? Tikamakhala ndi chifundo komanso makhalidwe amene tatchulawa, sitingachitire mwina koma kutonthoza ena. Paja Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chabwino chamumtima mwake, koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’chuma choipa chamumtima mwake.” (Mat. 12:34, 35) Kutonthoza abale ndi alongo athu omwe akumana ndi mavuto ndi njira yofunika kwambiri yomwe tingasonyezere kuti timawakonda. w23.11 10 ¶10-11

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lamlungu, August 31

Anthu ozindikira adzawamvetsetsa.​—Dan. 12:10.

Tiyenera kupempha Mulungu kuti atithandize kumvetsa ulosi wa m’Baibulo. Taganizirani chitsanzo ichi: Tayerekezerani kuti mukuyenda m’dera lachilendo koma mnzanu amene mwayenda naye akudziwa bwino deralo. Akudziwa bwino pamene muli komanso kumene msewu uliwonse ukulowera. Mosakayikira mungasangalale kuti mnzanuyo anavomera kuti muyende naye. Mofanana ndi zimenezi, Yehova akudziwa bwino nthawi yomwe tikukhalamoyi komanso zimene zichitike kutsogoloku. Choncho kuti tizimvetsa maulosi a m’Baibulo, modzichepetsa tiyenera kupempha Yehova kuti atithandize. (Dan. 2:28; 2 Pet. 1:19, 20) Mofanana ndi kholo lililonse lachikondi, Yehova amafuna kuti ana ake akhale ndi tsogolo labwino. (Yer. 29:11) Koma mosiyana ndi makolo athu, Yehova akhoza kuneneratu zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo molondola kwambiri. Iye analola kuti maulosi alembedwe m’Mawu ake ndi cholinga choti tizidziwa zinthu zofunika zisanachitike.—Yes. 46:10. w23.08 8 ¶3-4

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena